1 CCL Paulo mtumwi, osati wosankhidwa ndi anthu kapena kutumidwa ndi munthu ayi, koma Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate amene anamuukitsa Yesuyo kwa akufa, BSB BSB: Paul, an apostle—sent not from men nor by man, but by Jesus Christ and God the Father, who raised Him from the dead—
2 CCL pamodzi ndi abale onse amene ali nane, Kulembera mipingo ya ku Galatiya: BSB BSB: and all the brothers with me, To the churches of Galatia:
3 CCL Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu. BSB BSB: Grace and peace to you from God our Father and the Lord Jesus Christ,
4 CCL Yesuyo anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu kuti atipulumutse ku njira za moyo woyipa uno, molingana ndi chifuniro cha Mulungu ndi Atate athu. BSB BSB: who gave Himself for our sins to rescue us from the present evil age, according to the will of our God and Father,
5 CCL Ulemerero ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Ameni. BSB BSB: to whom be glory forever and ever. Amen.
7 CCL umene si Uthenga Wabwino konse. Pali anthu ena amene akukusokonezani komanso akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wa Khristu. BSB BSB: which is not even a gospel. Evidently some people are troubling you and trying to distort the gospel of Christ.
9 CCL Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, “Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa.” BSB BSB: As we have said before, so now I say again: If anyone is preaching to you a gospel contrary to the one you received, let him be under a curse!
10 CCL Kodi tsopano ndikufuna kukopa anthu kuti andivomereze, kapena Mulungu? Kapena ndikufuna kukondweretsa anthu? Ngati ine ndikanakhala kuti ndikufunabe kukondweretsa anthu, sindikanakhala mtumiki wa Khristu. BSB BSB: Am I now seeking the approval of men, or of God? Or am I striving to please men? If I were still trying to please men, I would not be a servant of Christ.
11 CCL Abale, ine ndikufuna kuti mudziwe, kuti Uthenga Wabwino umene ndinalalikira si ochokera kwa munthu ayi. BSB BSB: For I want you to know, brothers, that the gospel I preached was not devised by man.
12 CCL Ine sindinawulandire kuchokera kwa munthu aliyense, kapena kuphunzitsidwa; koma ndinawulandira mwa vumbulutso lochokera kwa Khristu. BSB BSB: I did not receive it from any man, nor was I taught it; rather, I received it by revelation from Jesus Christ.
14 CCL Ine ndinkapambana Ayuda ambiri a msinkhu wanga pochita za Chiyuda, ndipo ndinali wachangu koposa pa miyambo ya makolo athu. BSB BSB: I was advancing in Judaism beyond many of my contemporaries and was extremely zealous for the traditions of my fathers.
15 CCL Koma Mulungu, amene anandipatula ine ndisanabadwe, ndi kundiyitana mwachisomo chake, atakondweretsedwa BSB BSB: But when God, who set me apart from my mother’s womb and called me by His grace, was pleased
16 CCL kuvumbulutsa Mwana wake mwa ine, kuti ndikalalikire Khristuyo pakati pa anthu a mitundu ina, ine sindinapemphe nzeru kwa munthu aliyense. BSB BSB: to reveal His Son in me so that I might preach Him among the Gentiles, I did not rush to consult with flesh and blood,
17 CCL Ine sindinapite ku Yerusalemu kukaonana ndi amene anali atumwi ine ndisanakhale mtumwi. Mʼmalo mwake nthawi yomweyo ndinapita ku Arabiya ndi kubwereranso ku Damasiko. BSB BSB: nor did I go up to Jerusalem to the apostles who came before me, but I went into Arabia and later returned to Damascus.
20 CCL Ine ndikutsimikizira inu pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulemberani si zonama ayi. BSB BSB: I assure you before God that what I am writing to you is no lie.
21 CCL Pambuyo pake ndinapita ku Siriya ndi ku Kilikiya. BSB BSB: Later I went to the regions of Syria and Cilicia.
22 CCL Koma sindimadziwika ndi nkhope ku mipingo ya ku Yudeya imene ili mwa Khristu. BSB BSB: I was personally unknown, however, to the churches of Judea that are in Christ.
23 CCL Iwo anangomva mbiri yokha yakuti, “Munthu amene poyamba anatizunza ife, tsopano akulalikira chikhulupiriro chimene iyeyo nthawi ina anafuna kuchiwononga.” BSB BSB: They only heard the account: “The man who formerly persecuted us is now preaching the faith he once tried to destroy.”
24 CCL Ndipo iwo anayamika Mulungu chifukwa cha ine. BSB BSB: And they glorified God because of me.