2 CCL monga mmene zinaperekedwera kwa ife ndi iwo amene anaona poyambirira ndi atumiki a mawu. BSB BSB: just as they were handed down to us by the initial eyewitnesses and servants of the word.
3 CCL Popeza inenso ndafufuza mosamalitsa chilichonse kuyambira pachiyambi, zandikomera kukulemberani mwatsatanetsatane inu wolemekezeka Tiofilo, BSB BSB: Therefore, having carefully investigated everything from the beginning, it seemed good also to me to write an orderly account for you, most excellent Theophilus,
4 CCL kuti mudziwe bwinobwino zoona za zinthu zimene mwaphunzitsidwa. BSB BSB: so that you may know the certainty of the things you have been taught.
6 CCL Onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo amasunga malamulo ndi malangizo onse a Ambuye osalakwa konse. BSB BSB: Both of them were righteous in the sight of God, walking blamelessly in all the commandments and decrees of the Lord.
7 CCL Koma analibe ana chifukwa Elizabeti anali wosabereka; ndipo onse anali okalamba. BSB BSB: But they had no children, because Elizabeth was barren, and they were both well along in years.
8 CCL Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu, BSB BSB: One day while Zechariah’s division was on duty and he was serving as priest before God,
9 CCL Zakariyayo anasankhidwa mwa maere, monga mwa mwambo wa unsembe, kupita mʼNyumba ya Ambuye kukafukiza lubani. BSB BSB: he was chosen by lot, according to the custom of the priesthood, to enter the temple of the Lord and burn incense.
10 CCL Ndipo nthawi yofukiza lubani itafika, gulu lonse lopembedza linkapemphera kunja. BSB BSB: And at the hour of the incense offering, the whole congregation was praying outside.
11 CCL Kenaka mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye, atayimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizira. BSB BSB: Just then an angel of the Lord appeared to Zechariah, standing at the right side of the altar of incense.
12 CCL Zakariya ataona mngeloyo, anadzidzimuka ndipo anagwidwa ndi mantha. BSB BSB: When Zechariah saw him, he was startled and gripped with fear.
13 CCL Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane. BSB BSB: But the angel said to him, “Do not be afraid, Zechariah, because your prayer has been heard. Your wife Elizabeth will bear you a son, and you are to give him the name John.
14 CCL Ndipo adzakhala chimwemwe ndi chisangalalo kwa iwe, ndipo ambiri adzasangalala chifukwa cha kubadwa kwake, BSB BSB: He will be a joy and delight to you, and many will rejoice at his birth,
15 CCL chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa. BSB BSB: for he will be great in the sight of the Lord. He shall never take wine or strong drink, and he will be filled with the Holy Spirit even from his mother’s womb.
16 CCL Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo. BSB BSB: Many of the sons of Israel he will turn back to the Lord their God.
18 CCL Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.” BSB BSB: “How can I be sure of this?” Zechariah asked the angel. “I am an old man, and my wife is well along in years.”
19 CCL Mngeloyo anayankha kuti, “Ine ndine Gabrieli. Ndimayima pamaso pa Mulungu, ndipo ndatumidwa kwa iwe kudzakuwuza uthenga wabwinowu. BSB BSB: “I am Gabriel,” replied the angel. “I stand in the presence of God, and I have been sent to speak to you and to bring you this good news.
20 CCL Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.” BSB BSB: And now you will be silent and unable to speak until the day this comes to pass, because you did not believe my words, which will be fulfilled at their proper time.”
21 CCL Pa nthawiyi, anthu ankadikira Zakariya ndipo anadabwa chifukwa anatenga nthawi yayitali ali mʼNyumba ya Mulungu. BSB BSB: Meanwhile, the people were waiting for Zechariah and wondering why he took so long in the temple.
22 CCL Atatuluka sanathe kuyankhulana nawo. Anazindikira kuti anaona masomphenya mʼNyumbamo, chifukwa ankasonyeza zizindikiro kwa iwo koma sankatha kuyankhula. BSB BSB: When he came out and was unable to speak to them, they realized he had seen a vision in the temple. He kept making signs to them but remained unable to speak.
23 CCL Nthawi yake yotumikira itatha, anabwerera kwawo. BSB BSB: And when the days of his service were complete, he returned home.
24 CCL Zitatha izi, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pakati ndipo anadzibisa kwa miyezi isanu. BSB BSB: After these days, his wife Elizabeth became pregnant and for five months remained in seclusion. She declared,
25 CCL Iye anati, “Ambuye wandichitira izi, kuti mʼmasiku ano wandionetsera kukoma mtima kwake ndi kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.” BSB BSB: “The Lord has done this for me. In these days He has shown me favor and taken away my disgrace among the people.”
27 CCL kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya. BSB BSB: to a virgin pledged in marriage to a man named Joseph, who was of the house of David. And the virgin’s name was Mary.
28 CCL Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.” BSB BSB: The angel appeared to her and said, “Greetings, you who are highly favored! The Lord is with you.”
29 CCL Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere. BSB BSB: Mary was greatly troubled at his words and wondered what kind of greeting this might be.
30 CCL Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. BSB BSB: So the angel told her, “Do not be afraid, Mary, for you have found favor with God.
31 CCL Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. BSB BSB: Behold, you will conceive and give birth to a son, and you are to give Him the name Jesus.
32 CCL Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, BSB BSB: He will be great and will be called the Son of the Most High. The Lord God will give Him the throne of His father David,
33 CCL ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.” BSB BSB: and He will reign over the house of Jacob forever. His kingdom will never end!”
35 CCL Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. BSB BSB: The angel replied, “The Holy Spirit will come upon you, and the power of the Most High will overshadow you. So the Holy One to be born will be called the Son of God.
36 CCL Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. BSB BSB: Look, even Elizabeth your relative has conceived a son in her old age, and she who was called barren is in her sixth month.
37 CCL Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.” BSB BSB: For no word from God will ever fail.”
39 CCL Nthawi imeneyo anakonzeka ndipo anapita mofulumira ku mudzi wa ku mapiri a dziko la Yudeya, BSB BSB: In those days Mary got ready and hurried to a town in the hill country of Judah,
40 CCL kumene anakalowa mʼnyumba ya Zakariya nalonjera Elizabeti. BSB BSB: where she entered the home of Zechariah and greeted Elizabeth.
41 CCL Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. BSB BSB: When Elizabeth heard Mary’s greeting, the baby leaped in her womb, and Elizabeth was filled with the Holy Spirit.
42 CCL Anafuwula ndi mawu akulu kuti, “Ndiwe wodala pakati pa akazi, ndipo ndi wodala mwana amene udzabereke! BSB BSB: In a loud voice she exclaimed, “Blessed are you among women, and blessed is the fruit of your womb!
43 CCL Koma nʼchifukwa chiyani andikomera mtima kuti amayi a Ambuye anga abwere kwa ine? BSB BSB: And why am I so honored, that the mother of my Lord should come to me?
44 CCL Nthawi yomwe ndinamva mawu akulonjera kwanu, mwana anatakataka mʼmimba mwanga chifukwa cha chimwemwe. BSB BSB: For as soon as the sound of your greeting reached my ears, the baby in my womb leaped for joy.
45 CCL Wodala iye amene wakhulupirira kuti chimene Ambuye wanena kwa iye chidzakwaniritsidwa!” BSB BSB: Blessed is she who has believed that the Lord’s word to her will be fulfilled.”
47 CCL Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga, BSB BSB: and my spirit rejoices in God my Savior!
49 CCL pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu, dzina lake ndi loyera. BSB BSB: For the Mighty One has done great things for me. Holy is His name.
50 CCL Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye kufikira mibadomibado. BSB BSB: His mercy extends to those who fear Him, from generation to generation.
51 CCL Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake; Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo. BSB BSB: He has performed mighty deeds with His arm; He has scattered those who are proud in the thoughts of their hearts.
52 CCL Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu, koma wakweza odzichepetsa. BSB BSB: He has brought down rulers from their thrones, but has exalted the humble.
53 CCL Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino koma anachotsa olemera wopanda kanthu. BSB BSB: He has filled the hungry with good things, but has sent the rich away empty.
54 CCL Iye anathandiza mtumiki wake Israeli, pokumbukira chifundo chake. BSB BSB: He has helped His servant Israel, remembering to be merciful,
55 CCL Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse monga ananena kwa makolo athu.” BSB BSB: as He promised to our fathers, to Abraham and his descendants forever.”
56 CCL Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu ndipo kenaka anabwerera kwawo. BSB BSB: Mary stayed with Elizabeth for about three months and then returned home.
57 CCL Itakwana nthawi yoti Elizabeti abereke, anabereka mwana wamwamuna. BSB BSB: When the time came for Elizabeth to have her child, she gave birth to a son.
58 CCL Anansi ndi abale ake anamva kuti Ambuye anamuchitira chifundo chachikulu ndipo anakondwera naye pamodzi. BSB BSB: Her neighbors and relatives heard that the Lord had shown her great mercy, and they rejoiced with her.
59 CCL Pa tsiku lachisanu ndi chitatu anabwera ndi mwana kuti adzachitidwe mdulidwe, ndipo anafuna kumupatsa dzina la abambo ake Zakariya, BSB BSB: On the eighth day, when they came to circumcise the child, they were going to name him after his father Zechariah.
60 CCL koma amayi ake anayankhula nati, “Ayi, atchulidwe kuti Yohane.” BSB BSB: But his mother replied, “No! He shall be called John.”
61 CCL Iwo anati kwa iye, “Palibe mmodzi mwa abale ake amene ali ndi dzina limeneli.” BSB BSB: They said to her, “There is no one among your relatives who bears this name.”
62 CCL Pamenepo anapanga zizindikiro kwa abambo ake kuti adziwe dzina limene akanakonda kumutcha mwanayo. BSB BSB: So they made signs to his father to find out what he wanted to name the child.
63 CCL Iye anapempha poti alembepo, ndipo chodabwitsa kwa aliyense analemba kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” BSB BSB: Zechariah asked for a tablet and wrote, “His name is John.” And they were all amazed.
64 CCL Nthawi yomweyo pakamwa pake panatsekuka ndi lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula, nayamika Mulungu. BSB BSB: Immediately Zechariah’s mouth was opened and his tongue was released, and he began to speak, praising God.
65 CCL Anansi onse anachita mantha kwambiri, ndipo ku madera onse a kumapiri a Yudeya, anthu anayankhula zinthu zonsezi. BSB BSB: All their neighbors were filled with awe, and people throughout the hill country of Judea were talking about these events.
66 CCL Aliyense amene anamva izi anadabwa nazo nafunsa kuti, “Kodi mwana uyu adzakhala wotani?” Pakuti dzanja la Ambuye lili pa iye. BSB BSB: And all who heard this wondered in their hearts and asked, “What then will this child become?” For the Lord’s hand was with him.
67 CCL Abambo ake, Zakariya, anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenera kuti, BSB BSB: Then his father Zechariah was filled with the Holy Spirit and prophesied:
68 CCL “Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake. BSB BSB: “Blessed be the Lord, the God of Israel, because He has visited and redeemed His people.
69 CCL Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife mu nyumba ya mtumiki wake Davide. BSB BSB: He has raised up a horn of salvation for us in the house of His servant David,
70 CCL (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera), BSB BSB: as He spoke through His holy prophets, those of ages past,
71 CCL chipulumutso kuchoka kwa adani athu ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida, BSB BSB: salvation from our enemies and from the hand of all who hate us,
72 CCL kuonetsa chifundo kwa makolo athu ndi kukumbukira pangano lake loyera, BSB BSB: to show mercy to our fathers and to remember His holy covenant,
73 CCL lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu: BSB BSB: the oath He swore to our father Abraham, to grant us
74 CCL kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu, ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha, BSB BSB: deliverance from hostile hands, that we may serve Him without fear,
75 CCL mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse. BSB BSB: in holiness and righteousness before Him all the days of our lives.
76 CCL “Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba; pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake, BSB BSB: And you, child, will be called a prophet of the Most High; for you will go on before the Lord to prepare the way for Him,
77 CCL kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo, BSB BSB: to give to His people the knowledge of salvation through the forgiveness of their sins,
78 CCL chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba, BSB BSB: because of the tender mercy of our God, by which the Dawn will visit us from on high,
79 CCL kuwalira iwo okhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa, kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere.” BSB BSB: to shine on those who live in darkness and in the shadow of death, to guide our feet into the path of peace.”
80 CCL Ndipo mwanayo anakula nakhala wamphamvu mu mzimu; ndipo anakhala ku chipululu mpaka pamene anaonekera poyera mu Israeli. BSB BSB: And the child grew and became strong in spirit; and he lived in the wilderness until the time of his public appearance to Israel.